Mkulu wa gulu la Citizen For Transformation (CFT) yemwenso ndi nduna ya Civic Education ndi national unity olemekeza a Timothy Mtambo atsutsa kwamtuu wagalu kuti sapikisana nawo mpando wa nyumba ya malamulo ku Karonga central.
Mchikalata chomwe bungweli lasindikiza lero chatsimikiza kuti mtsogoleri wawoyu alibe chidwi choimira ku derali.
Chikalachi chati bungwe la CFT silandale ngati momwe ena akuganizira.
Bungwe la chisankho la Malawi Electoral commission (MEC) lidalengeza kuti ku dera la Karonga central tsopano kulibe phungwe kutsatira imfa ya Dr. Cornelius Mwalwanda yemwe anali phungu wa deralo.
Dr. Mwalwanda anamwalira atadwala Covid 19.
Mphekesera zomwe zatipeza, mtsogoleri wakale wachipani cha AFORD a Frank Mwenefumbo watuluka mchipanicho ndipo zikumveka kuti akufuna kulowa pakati pa UTM ndi MCP, Pofuna kupikisana nao pa mpando wa phungu wa nyumba ya malamulo ku karonga central.