Bungwe la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) layamba zokonzekera zionetsero zofuna kuwumiliza bungwe la Public Appointments Committee (PAC) kuti lilimbe ntchito a Martha Chizuma.
Zionetserozi zichitika pa 18, May mwezi uno.Mwa zina bungweli lapangitsa ma T-shirt omwe atazavalidwe pa tsikulo.

Anthu ochuluka mdziko muno alankhula pa za ganizo lomwe bungwe la HRDC likufuna kuchita.
Ena ati bungweli likadakhala la nzeru likadachititsa zionetsero zomuuza mtsogoleri wa dziko lino kuti alembe ntchito anthu 1 million monga mmene adalonjezera pa nthawi ya Kampeni zomwe mpaka pano sizinachitike.