Bungwe loonetsesa kuti ziphuphu ndi katangale palibe mdziko muno la Anti Corruption Bureau lati lionetsesa komanso kupanga kafukufuku kuti lidziwe ngati ma basi omwe anapelekedwa ndi mtsogoleri wakale wa dziko lino a professor Arthur Peter Mutharika ku matimu a Nyasa Big Bullets komanso Be forward Mighty Wanderers anagulidwadi ku kampani ya Rashy Motors.

Poyankhula kwa olemba nkhani, mkulu wa bungwe la ACB a Reyneck Matemba anati auza matimuwa kuti afotokozepo za yemwe ali mwini wa mabasiwa ndipo kuti akamadzasintha umwini ku Director of Road Traffic adzawadziwitse kuti adzalondololeze bwino za nkhaniyi.
Koma atafunsidwa , akuluakulu a matimuwa omwe ndi a Albert Chigoga a timu ya Bullets komanso a Victor Maunde a Wanderers anapempha kuti apatsidwe kaye nthawi asanayankhulepo.
Nkhaniyi ikudza pomwe zikumveka kuti ma basiwa anatengedwa ku nthambi ya Malawi Post Corporation osati zomwe anayankhula a Mutharika kuti anagula ma basiwa ndi ndalama zokwana K250 miliyoni kuchokera ku kampani ya Rashy Motors.
A Mutharika analonjeza ma basi ku matimu a Wanderers komanso Bullets pomwe amakhazikitsa ntchito yomanga mabwalo a matimu awiriwa.